Mzuzu
Mzuzu ndi mzinda mu dziko la Malaŵi. Mzindawu umapezeka ku mpoto kwa dziko la Malawi ndipo ndi tawuni yayikulu mu dera la kumpoto. Mzuzu ndi mzinda wachitatu kukula kutrngela kuchulukwa kwa anthu mu dziko la Malawi. Mzindawu wuli ndi anthu okwana 221,272 ndi ana asukulu okwana 20,000 omwe amaphunzira ku sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu univesite. Anthu okwana 1.7 miliyoni amakhalammadera ozungulira mzindawu. Mzindawu uli mu boma la Mzimba ndipo uli mdera lomwe ndi mchigwa cha phiri la Viphya. Ndipo madera oyandikila derali muli malo achitikira nthcito za ulimi monga tiyi, rabala ndi khofi. Malo a nkhalango a Viphya anali malo akulu a nkhalango yodzalida ndi anthu. madera otchuka mzindawu ndi Chimaliro, Katoto, Chibavi, Luwinga, Masasa ndi Zolozolo.